Lemba la chaka
M'patseni Yehova ulemelero
woyenera dzina lake.
- Salimo 96: 8
M'patseni Yehova ulemelero
woyenera dzina lake.
- Salimo 96: 8
Tiyerekezere kuti anthu onse m'mudzi akupangirani upo ndipo akukuthamangitsani. Ndipo mutapita kwa mfumu, mukuuzidwa kuti “musaope ndipo palibe chilichonse chomwe chingakuchitikireni”, kodi mungamve bwanji? Mukhonza kukhala olimba mtima chifukwa mwalimbikitsidwa ndi munthu yemwe ali ndi udindo waukulu komanso wakupatsani chiyembekezo ndi chidaliro choti mukhala otetezeka. Ndi m'meneso Yehova amatilimbitsira mtima pa mavuto omwe timakumana nawowa. Pa lemba la Yesaya 54:17 Yehova anati: “Palibe chida chomwe chidzativulaze kapena kupambana (kutilepheretsa kutumikira Yehova kapena kutichotsa pa ubwenzi wathu ndi IYE).” Apatu sananene kuti palibe chida chomwe chidzapangidwe koma anati chida chomwe chingazapangidwecho sichizapambana.
Kodi ndi zida ziti zimene Satana amagwiritsa ntchito nanga nchifukwa chiyani amalimbana ndi Akhristu Oona?
Anthu ena amawanamiza anzawo omwe akufuna kukhala a mboni kuti 'samakhala ndi mwayi wa mdzikoli' ndipo ena amafika ponena kuti 'ana awo azingofa'. Kuwonjezera pamenepo, ena angamapekenso nkhani zina zoipitsa gulu la Yehova. Tisaiwale kuti satana anaputsitsa Adamu ndi Hava mnjira ngati imeneyi m'munda wa Edeni ndipo ndi zomwe angachitenso kwa ife. Kumbukiraninso kuti Adamu ndi Hava anaputsitsidwa ali angwiro, ndiye kuli bwanji opanda ungwirofe. Tiyenera kukhala osamala kwambiri ndi mabodza a oipayu.
Anthu ena amaopsezedwa kuti ngati angakhale a mboni athamangitsidwa m'mudzi kapenanso banja litha. Ana a mboni ku sukulu amauzidwanso kuti 'ngati saimba nyimbo ya fuko kapena kuchita sawatcha mbendera alandira chilango kapena kuchotsedwa sukulu'. Madokotala ena amaopsezanso a mboni omwe akukana kuikidwa magazi kuti akhonza kufa.
Ngati takana kuchita zomwe ena akuchita monga kusainira za ndale, kuvota, kukana ziphuphu kapena mwambo ulionse tingathe kuchititsidwa manyazi. Nthawi zina madokotala ndi ma patient angatiseke ngati takana kuikidwa magazi.
Anthu ena angasekeredwe mndende chifukwa cha choonadi kuti tiope kapena kusiya umboni. Abale ena akhala mndende kwa zaka zoposa 20, ku Elitrea, Singapore ndi ku South Korea, koma sanasiye choonadi ndipo sanalole chilichonse kuwalepheretsa kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.
AMboni za Yehova m'Malawi anazunzidwa kwa nthawi yaitali kuti asiye chikhulupiliro chawo koma sanasiye.
Mnthawi ya atumwi, Satana anagwiritsa ntchito Ayuda kuti aphe Sitefano. Anthu enanso anaphedwa poopseza akhristu osalawo kuti asiye kuchitira umboni za Uthenga Wabwino
Tizipempha kuti atithandize ndi abale omwe akuzunzidwawo. Uthenga wabwino ukulalikidwabe ku Russia ngakhale chizunzo chikupitilira. Tiziyembekezera kuti nthawi ina tidzakumana ndi zimenezi ndipo tizikumbukira kuti nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake ngati m'mene wakhala akuchitira m'mbuyomo.